Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 7:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Potero sindidzaletsa pakamwa panga;Ndidzalankhula popsinjika mumzimu mwanga;Ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.

12. Ndine nyanja kodi, kapena cinjoka ca m'nyanja,Kuti Inu mundiikira odikira?

13. Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,Pogona panga padzacepsa condidandaulitsa;

14. Pamenepo mundiopsa ndi maloto,Nimundicititsa mantha ndi masomphenya;

15. Potero moyo wanga usankha kupotedwa,Ndi imfa, koposa mafupa anga awa.

16. Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo cikhalire;Mundileke; pakuti masiku anga ndi acabe.

17. Munthu ndani kuti mumkuze,Ndi kuti muike mtima wanu pa iye,

18. Ndi kuti muceze naye m'mawa ndi m'mawa,Ndi kumuyesa nthawi zonse?

19. Mukana kundicokera kufikira liti,Kapena kundileka mpaka nditameza dobvu?

Werengani mutu wathunthu Yobu 7