Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 42:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yobu anayankha Mulungu, nati,

2. Ndidziwa kuti mukhoza kucita zonse,Ndi kuti palibe coletsa colingirira canu ciri conse,

3. Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu?Cifukwa cace ndinafotokozera zimene sindinazizindikira,Zondidabwiza, zosazidziwa ine,

4. Tamveranitu, ndidzanena ine,Ndidzakufunsani, mundidziwitse.

5. Kumva ndidamva mbiri yanu,Koma tsopano ndikupenyani maso;

6. Cifukwa cace ndekha ndidzinyansa, ndi kulapaM'pfumbi ndi mapulusa.

7. Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenera coyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu.

8. Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzambvomereza iyeyu, kuti ndisacite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera coyenera monga ananena mtumiki Yobu.

9. Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofara wa ku Naama, nacita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anabvomereza Yobu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 42