Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 35:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,

2. Kodi muciyesa coyenera,Umo mukuti, Cilungamo canga ciposa ca Mulungu,

3. Pakuti munena, Upindulanji naco?Posacimwa ndinapindula ciani cimene sindikadapindula pocimwa?

4. Ndidzakuyankhani,Ndi anzanu pamodzi ndi inu.

5. Yang'anani kumwamba, nimuone,Tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 35