Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 32:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.

5. Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.

6. Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati,Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.

7. Ndinati, Amisinkhu anene,Ndi a zaka zocuruka alangize nzeru.

8. Koma m'munthu muli mzimu,Ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.

9. Akulu sindiwo eni nzeru,Ndi okalamba sindiwo ozindikira ciweruzo.

10. Cifukwa cace ndinati, Ndimvereni ine,Inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine.

11. Taonani, ndinalindira mau anu,Ndinacherera khutu zifukwa zanu,Pofunafuna inu ponena.

12. Inde ndinasamalira inu;Koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu,Kapena wakumbwezera mau pakati painu.

13. Msamati, Tapeza nzeru ndife,Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai;

Werengani mutu wathunthu Yobu 32