Ndipo Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi anayankha, nati,Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba;Cifukwa cace ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine.