Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 32:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pace pa iye mwini.

2. Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakeli wa ku Buzi, wa cibale ca Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.

3. Adapsa mtima pa mabwenzi ace atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa.

4. Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa.

5. Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima.

Werengani mutu wathunthu Yobu 32