Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 26:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Analembera madziwo malire,Mpaka polekeza kuunika ndi mdima.

11. Mizati ya thambo injenjemera,Ndi kudabwa pa kudzudzula kwace.

12. Mwa mphamvu yace agwetsa nyanja bata;Ndipo mwa luntha lace akantha kudzikuza kwace.

13. Mwa mzimu wace anyezimiritsa thambo;Dzanja lace linapyoza njoka yothawayo.

14. Taonani, awa ndi malekezero a njira zace;Ndi cimene tikumva za Iye ndi cinong'onezo cacing'ono;Koma kugunda kwa mphamvu yace akuzindikiritsa ndani?

Werengani mutu wathunthu Yobu 26