1. Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ace?
2. Alipo akusendeza malire;Alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.
3. Akankhizira kwao buru wa amasiye,Atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale cikole.
4. Apambukitsa aumphawi m'njira;Osauka a padziko abisala pamodzi.
5. Taonani, ngati mbidzi za m'cipululuAturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya;Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao.
6. Atema dzinthu zao m'munda;Natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.
7. Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala,Alibe copfunda pacisanu.
8. Abvumbwa ndi mvula kumapiri,Nafukata thanthwe posowa pousapo.