Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 24:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo?Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ace?

2. Alipo akusendeza malire;Alanda gulu la zoweta, nazidyetsa.

3. Akankhizira kwao buru wa amasiye,Atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale cikole.

4. Apambukitsa aumphawi m'njira;Osauka a padziko abisala pamodzi.

5. Taonani, ngati mbidzi za m'cipululuAturukira ku nchito zao, nalawirira nkufuna cakudya;Cipululu ciwaonetsera cakudya ca ana ao.

6. Atema dzinthu zao m'munda;Natola khunkha m'munda wampesa wa woipa.

7. Agona amarisece usiku wonse opanda cobvala,Alibe copfunda pacisanu.

8. Abvumbwa ndi mvula kumapiri,Nafukata thanthwe posowa pousapo.

9. Akwatula wamasiye kubere,Natenga cikole cobvala ca osauka;

10. Momwemo ayenda amarisece opanda cobvala,Nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala.

11. M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta;Aponda mphesa moponderamo, namva ludzu.

12. M'mudzi waukuru anthu abuula alinkufa;Ndi moyo wa iwo olasidwa upfuula;Koma Mulungu sasamalira coipaco.

13. Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika,Sadziwa njira zace,Sasunga mayendedwe ace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 24