Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 23:6-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?Iai, koma akadandicherera khutu.

7. Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.

8. Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;Kapena m'mbuyo sindimzindikira;

9. Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;Akabisala kulamanja, sindimuona,

10. Koma adziwa njira ndilowayi;Atandiyesa ndidzaturuka ngati golidi.

11. Phazi langa lagwiratu moponda Iye,Ndasunga njira yace, wosapambukamo.

12. Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yace;Ndasungitsa mau a pakamwa pace koposa lamulo langa langa.

13. Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani?Ndi ici cimene moyo wace ucifuna acicita.

14. Pakuti adzacita condiikidwiratu;Ndipo zambiri zotere ziri ndi Iye.

15. Cifukwa cace ndiopsedwa pankhope pace;Ndikalingirira, ndicita mantha ndi Iye.

16. Pakuti Mulungu walefula mtima wanga,Ndi Wamphamvuyonse wandiopsa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 23