Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 23:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Yobu anayankha, nati,

2. Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa;Kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwace.

3. Ha! ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu,Kuti ndifike ku mpando wace!

4. Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pace,Ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano.

5. Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine,Ndikadazindikira cimene akadanena nane.

6. Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yace yaikuru?Iai, koma akadandicherera khutu.

7. Apo woongoka mtima akadatsutsana naye;Ndipo ndikadapulumuka cipulumukire kwa Woweruza wanga.

8. Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye;Kapena m'mbuyo sindimzindikira;

9. Akacita Iye kulamanzere, sindimpenyerera;Akabisala kulamanja, sindimuona,

Werengani mutu wathunthu Yobu 23