Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 2:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, cinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda cifukwa.

4. Nayankha Satana, nati kwa Yehoya, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wace.

5. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza pfupa lace ndi mnofu wace, ndipo adzakucitirani mwano pamaso panu.

6. Ndipo Yehova anati kwa Satana. Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wace wokha uuleke.

7. Naturuka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zironda zowawa, kuyambira ku phazi lace kufikira pakati pamutu pace.

8. Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'mapulusa.

9. Pamenepo mkazi wace ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? citira Mulungu mwano, ufe.

10. Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? pa ici conse Yobu sanacimwa ndi milomo yace.

11. Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za coipa ici conse cidamgwera, anadza, yense kucokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa.

Werengani mutu wathunthu Yobu 2