Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 17:2-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Zoonadi, ali nane ondiseka;Ndi diso langa liri cipenyere m'kundiwindula kwao.

3. Mupatse cigwiriro tsono, mundikhalire cikole Inu nokha kwanu;Ndani adzapangana nane kundilipirira?

4. Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;Cifukwa cace simudzawakuza.

5. Iye wakupereka mabwenzi ace kuukapolo,M'maso mwa ana ace mudzada.

6. Anandiyesanso nthanthi za anthu;Ndipo ndakhala ngati munthu womthira malobvu pankhope pace.

Werengani mutu wathunthu Yobu 17