10. Koma munthu akufa atacita liondeondeInde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti?
11. Madzi acoka m'nyanja,Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;
12. Momwemo munthu agona pansi, osaukanso;Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,Kapena kuutsidwa pa tulo tace.
13. Ha! mukadandibisa kumanda,Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.
14. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,Mpaka kwafika kusandulika kwanga,
15. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;Mukadakhumba nchito ya manja anu.
16. Koma tsopano muwerenga maponda mwanga;Kodi simuyang'anitsa cimo langa?
17. Colakwa canga caikidwa m'thumba lokomedwa cizindikilo;Ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.
18. Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;Ndi thanthwe lisunthika m'malo mwace;
19. Madzi anyenya miyala;Zosefukira zao zikokolola pfumbi la nthaka;Ndipo muononga ciyembekezo ca munthu.
20. Mumlaka cilakire, napita iye;Musintha nkhope yace, mumuuza acoke.
21. Ana ace aona ulemu osadziwa iye;Napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.
22. Koma thupi lace limuwawira yekha,Ndi mtima wace umliritsa yekha.