Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 14:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma munthu akufa atacita liondeondeInde, munthu apereka mzimu wace, ndipo ali kuti?

11. Madzi acoka m'nyanja,Ndi mtsinje ukuphwa, nuuma;

12. Momwemo munthu agona pansi, osaukanso;Kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso,Kapena kuutsidwa pa tulo tace.

13. Ha! mukadandibisa kumanda,Mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu.Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.

14. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga,Mpaka kwafika kusandulika kwanga,

15. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani;Mukadakhumba nchito ya manja anu.

16. Koma tsopano muwerenga maponda mwanga;Kodi simuyang'anitsa cimo langa?

17. Colakwa canga caikidwa m'thumba lokomedwa cizindikilo;Ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga.

18. Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha;Ndi thanthwe lisunthika m'malo mwace;

19. Madzi anyenya miyala;Zosefukira zao zikokolola pfumbi la nthaka;Ndipo muononga ciyembekezo ca munthu.

Werengani mutu wathunthu Yobu 14