Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 10:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma izi munazibisa mumtima mwamu;Ndidziwa kuti ici muli naco:

14. Ndikacimwa mundipenya;Ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.

15. Ndikakhala woipa, tsoka ine;Ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutuwanga;Ndadzazidwa ndi manyazi, Koma penyani kuzunzika kwanga.

16. Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango;Mubweranso ndi kudzionetsera modabwiza kwa ine.

17. Mundikonzeranso mboni zonditsutsa,Ndi kundicurukitsira mkwiyo wanu;Nkhondo yobwereza-bwereza yandigwera.

18. Potero munandibadwitsa cifukwa ninji?Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso.

19. Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala;Akadanditenga pobadwapo kumka nane kumanda.

20. Masiku anga satsala owerengeka nanga? lindani,Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono,

21. Ndisanacoke kumka kumene sindikabweranso,Ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa;

22. Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani,Dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka,Kumene kuunika kukunga mdima.

Werengani mutu wathunthu Yobu 10