Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 9:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efraimu ndi okhala m'Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima,

10. Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.

11. Cifukwa cace Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ace;

12. Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israyeli ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.

13. Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.

14. Cifukwa cace Yehova adzadula mutu wa Israyeli ndi mcira wace; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi.

15. Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mcira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 9