Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 9:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Pakuti gori la katundu wace, ndi mkunkhu wa paphewa pace, ndodo ya womsautsa, inu mwazityola monga tsiku la Midyani.

5. Pakuti zida zonse za mwamuna wobvala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zobvala zobvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.

6. Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

7. Za kuenjezera ulamuliro wace, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wacifumu wa Davide, ndi pa ufumu wace, kuukhazikirsa, ndi kuucirikiza ndi ciweruziro ndi cilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Cangu ca Yehova wa makamu cidzacita zimenezi.

8. Ambuye anatumiza mau kwa Yakobo, ndipo anatsikira pa Israyeli.

9. Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efraimu ndi okhala m'Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima,

10. Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 9