Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 9:19-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wocitira mbale wace cisoni.

20. Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wace wa iye mwini.

21. Manase adzadya Efraimu ndi Efraimu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 9