Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 7:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Iye adzadya mafuta ndi uci, pamene adziwa kukana coipa ndi kusankha cabwino.

16. Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana coipa ndi kusankha cabwino, dziko limene mafumu ace awiri udana nao lidzasyidwa.

17. Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efraimu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asuri.

18. Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzayimbira mluzu cimphanga ciri m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Aigupto, ndi njuci iri m'dziko la Asuri.

19. Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.

20. Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m'mapazi, ndi lumo lobwereka liri tsidya lija la Nyanja, kunena mfumu ya Asuri; ndilo lidzamarizanso ndebvu.

21. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri;

22. ndipo padzakhala, cifukwa ca kucuruka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uci adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.

23. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti pali ponse panali mipesa cikwi cimodzi ya mtengo wace wa ndalama cikwi cimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.

24. Munthu adzafikako ndi mibvi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga.

25. Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako cifukwa ca kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 7