Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 64:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;

2. monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu,

3. Pamene Inu munacita zinthu zoopsya, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.

4. Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira nchito iye amene amlindirira Iye.

5. Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nacita cilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinacimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?

6. Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse ziri ngati cobvala codetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.

7. Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikangamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 64