Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 63:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndani uyu alinkudza kucokera ku Edomu, ndi zobvala zonika zocokera ku Bozira? uyu wolemekezeka m'cobvala cace, nayenda mu ukuru wa mphamvu zace? Ndine amene ndilankhula m'colungama, wa mphamvu yakupulumutsa,

2. Cophimba cako cifiiriranji, ndi zobvala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa?

3. Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga: ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zobvala zanga; ndipo ndadetsa copfunda canga conse.

4. Pakuti tsiku lakubwezera liri mumtima mwanga, ndi caka ca kuombola anthu anga cafika.

5. Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 63