19. Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
20. Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.
21. Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala colowa cao ku nthawi zonse, nthambi yooka Ine, nchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.
22. Wamng'ono adzasanduka cikwi, ndi wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ici m'nthawi yace.