Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 6:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.

9. Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa.

10. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, naciritsidwe.

11. Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,

12. ndipo Yehova wasunthira anthu kutari, ndi mabwinja adzacuruka pakati pa dziko.

13. Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kacere, ndi monganso thundu, imene tsinde lace likhalabe ataigwetsa; cotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 6