Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wacifumu wautari, ndi wotukulidwa, ndi zobvala zace zinadzala m'Kacisi.

2. Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yace, awiri naphimba nao mapazi ace, awiri nauluka nao.

3. Ndipo wina anapfuula kwa mnzace, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wace.

4. Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anapfuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.

5. Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! cifukwa ndathedwa; cifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; cifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.

6. Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m'dzanja mwace, limene analicotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 6