Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 59:5-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo.

6. Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwao.

7. Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m'njira mwao.

8. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe ciweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; ali yense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.

9. Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.

10. Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tipunthwa usana monga m'cizirezire; tiri m'malo amdima ngati akufa.

11. Tonse tibangula ngati zirombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira ciweruziro koma palibe; tiyang'anira cipulumutso koma ciri patari ndi ife.

12. Pakuti zolakwa zathu zacuruka pamaso pa Inu, ndipo macimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu ziri ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;

13. ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu, kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga oturuka mumtima.

14. Ndipo ciweruziro cabwerera m'mbuyo, ndi cilungamo caima patari; pakuti coona cagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 59