Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.