Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 59:3-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa.

4. Palibe woturutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwacabe, nanena zonama; iwo atenga kusayeruzika ndi kubala mphulupulu,

5. Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo.

6. Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwao.

7. Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m'njira mwao.

8. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe ciweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; ali yense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.

9. Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 59