Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 59:11-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Tonse tibangula ngati zirombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira ciweruziro koma palibe; tiyang'anira cipulumutso koma ciri patari ndi ife.

12. Pakuti zolakwa zathu zacuruka pamaso pa Inu, ndipo macimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu ziri ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;

13. ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu, kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga oturuka mumtima.

14. Ndipo ciweruziro cabwerera m'mbuyo, ndi cilungamo caima patari; pakuti coona cagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.

15. Inde coona cisoweka; iye amene asiya coipa, zifunkhidwa zace; ndipo Yehova anaona ici, ndipo cidamuipira kuti palibe ciweruzo.

16. Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; cifukwa cace mkono wace wace unadzitengera yekha cipulumutso; ndi cilungamo cace cinamcirikiza.

17. Ndipo anabvala cilungamo monga cida ca pacifuwa, ndi cisoti ca cipulumutso pamutu pace; nabvala zobvala zakubwezera cilango, nabvekedwa ndi cangu monga copfunda,

18. Monga mwa nchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ace ukali, nadzabwezera adani ace cilango; nadzabwezeranso zisumbu cilango.

19. Comweco iwo adzaopa dzina la Yehova kucokera kumadzulo, ndi ulemerero wace kumene kuturukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati cigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 59