Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 59:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Tonse tibangula ngati zirombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira ciweruziro koma palibe; tiyang'anira cipulumutso koma ciri patari ndi ife.

12. Pakuti zolakwa zathu zacuruka pamaso pa Inu, ndipo macimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu ziri ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;

13. ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu, kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga oturuka mumtima.

14. Ndipo ciweruziro cabwerera m'mbuyo, ndi cilungamo caima patari; pakuti coona cagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.

15. Inde coona cisoweka; iye amene asiya coipa, zifunkhidwa zace; ndipo Yehova anaona ici, ndipo cidamuipira kuti palibe ciweruzo.

16. Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; cifukwa cace mkono wace wace unadzitengera yekha cipulumutso; ndi cilungamo cace cinamcirikiza.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 59