10. Alonda ace ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agaru acete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.
11. Inde agaru ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira ku njira zao, yense kutsata phindu lace m'dera lace.
12. Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta cakumwa caukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikuru loposa ndithu.