12. Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.
13. Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
14. M'cilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutari ndi cipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutari ndi mantha, pakuti sadzafika cifupi ndi iwe.
15. Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; amene ali yense adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa cifukwa ca iwe.
16. Taona, ndalenga wacipala amene abvukuta moto wamakala, ndi kuturutsamo cida ca nchito yace; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.
17. Palibe cida cosulidwira iwe cidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'ciweruzo udzalitsutsa. Ici ndi colowa ca atumiki a Yehova, ndi cilungamo cao cimene cifuma kwa Ine, ati Yehova.