Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 54:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yimba, iwe wouma, amene sunabala; yimba zolimba ndi kupfuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa acuruka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.

2. Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsaru za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.

3. Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu colowa cao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.

4. Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.

5. Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lace; ndi Woyera wa Israyeli ndiye Mombolo wako; Iye adzachedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.

6. Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wocotsedwa, ati Mulungu wako.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 54