Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 51:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumcurukitsa.

3. Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ace onse abwinja; ndipo wasandutsa cipululu cace ngati Edene, ndi nkhwangwara yace ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.

4. Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kundicherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzacokera kwa ine, ndipo ndidzakhazikitsa ciweruziro canga cikhale kuunika kwa anthu.

5. Cilungamo canga ciripafupi, cipulumutso canga camuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.

6. Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko; pakuti kumwamba kudzacoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati copfunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa cimodzimodzi; koma cipulumutso canga cidzakhala ku nthawi lonse, ndi cilungamo canga sicidzacotsedwa.

7. Mverani Ine, inu amene mudziwa cilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope citonzo ca anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.

8. Pakuti njenjete idzawadya ngati copfunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma cilungamo canga cidzakhala ku nthawi zonse, ndi cipulumutso canga ku mibadwo yonse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 51