Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 5:15-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wochuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;

16. koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.

17. Pamenepo ana a nkhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zacilendo zidzadyapo.

18. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;

19. amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize nchito yace kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israyeli uyandikire, udze kuti tiudziwe!

20. Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!

21. Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ocenjera!

22. Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali;

23. amene alungamitsa woipa pa cokometsera mlandu, nacotsera wolungama cilungamo cace!

24. Cifukwa cace monga ngati lilime la moto likutha ciputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wobvunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati pfumbi; cifukwa kuti iwo akana cilamulo ca Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israyeli.

25. Cifukwa cace mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ace, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lace, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.

26. Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutari mbendera, nadzawayimbira mluzu, acokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msanga msanga;

27. palibe amene adzalema, kapena adzapunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'cuuno mwao silidzamasuka, kapena comangira ca nsapato zao sicidzaduka;

28. amene mibvi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kabvumvulu;

29. kubangula kwao kudzafana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naicotsa bwino opanda wakupulumutsa.

30. Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 5