Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 48:3-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinaturuka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazicita izo, ndipo zinaoneka.

4. Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako liri mtsempha wacitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;

5. cifukwa cace ndinakudziwitsa ici kuyambira kale; cisanaoneke ndinakusonyeza ico, kuti iwe unganene, Fano langa lacita izo, ndi cifanizito canga cosema, ndi cifaniziro canga coyenga zinazilamulira.

6. Iwe wacimva taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzacinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kucokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.

7. Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.

8. Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde, kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wacita mwaciwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa cibadwire.

9. Cifukwa ca dzina langa ndidzacedwetsa mkwiyo wanga, ndi cifukwa ca kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakucotse.

10. Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.

11. Cifukwa ca Ine ndekha, cifukwa ca Ine ndekha ndidzacita ici, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.

12. Mverani Ine, Yakobo ndi Israyeli, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womariza.

13. Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.

14. Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzacita kufuna kwace pa Babulo, ndi mkono wace udzakhala pa Akasidi.

15. Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yace.

16. Idzani inu cifupi ndi Ine, imvani ici; kuyambira pa ciyambi sindinanene m'tseri; ciyambire zimenezi, Ine ndiripo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wace.

17. Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israyeli, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.

18. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi cilungamo cako monga mafunde a nyanja;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 48