Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 47:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsika, ukhale m'pfumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babulo; khala pansi popanda mpando wacifumu, mwana wamkazi wa Akasidi, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.

2. Tenga mipero, nupere ufa; cotsa cophimba cako, bvula copfunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.

3. Marisece ako adzakhala osapfundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzacita kubwezera, osasamalira munthu.

4. Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lace, Woyera wa Israyeli.

5. Khala iwe cete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Akasidi; pakuti sudzachedwanso mkazi wa maufumu.

6. Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa colowa canga, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera cifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 47