Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 46:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.

2. Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende.

3. Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israyeli, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani cibadwire;

4. ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.

5. Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?

6. Amene ataya golidi, namturutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golidi; iye napanga nazo mlungu; iwo agwada pansi, inde alambira.

7. Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwace, nukhala ciriri; pamalo pacepo sudzasunthika; inde, wina adzaupfuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zobvuta zace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 46