Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 40:20-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungabvunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika.

21. Kodi inu simunadziwe? kodi inu simunamve? kodi sanakuuzani inu ciyambire? kodi inu simunadziwitse ciyambire mayambiro a dziko lapansi?

22. Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekerezo a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati cinsaru, naliyala monga hema wakukhalamo;

23. amene asandutsa akalonga kuti akhale acabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pace,

24. Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kabvumvulu awacotsa monga ciputu.

25. Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 40