Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 39:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nthawi imeneyo Merodakibaladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babulo, anatumiza akalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nacira.

2. Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yace ya cuma, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba yonse ya zida zace, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zace; munalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'dziko lace lonse, kamene Hezekiya sanawaonetsa.

3. Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo acokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo acokera ku dziko lakutari, kudza kwa ine, kunena ku Babulo.

4. Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona ciani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa cuma canga, kamene ine sindinawaonetse.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 39