Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 38:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Kodi ndidzanena ciani?Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wacita ici;Ine ndidzayenda cete zaka zanga zonse,Cifukwa ca zowawa za moyo wanga.

16. Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo.Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga;Cifukwa cace mundiciritse ine,Ndi kundikhalitsa ndi moyo.

17. Taonani, ndinali ndi zowawa zazikuru,Cifukwa ca mtendere wanga;Koma Inu mokonda moyo wanga,Munaupulumutsa m'dzanja la cibvundi,Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu macimo anga onse.

18. Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu;Imfa singakulemekezeni;Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.

19. Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero;Atate adzadziwitsa ana ace zoona zanu.

20. Yehova ndiye wondipulumutsa ine;Cifukwa cace tidzayimba nyimbo zanga, ndi zoyimba zazingweMasiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.

21. Ndipo Yesaya adati, Atenge mbulu wankhuyu, auike papfundo, Ndipo iye adzacira.

22. Hezekiya anatinso, Cizindikilo nciani, kuti ndidzakwera kunka ku nyumba ya Yehova?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 38