Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 38:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11. Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

12. Pokhala panga pacotsedwa, pandisunthikira monga hema wambusa;Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba;Iye adzandidula ine poomberapo;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

13. Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anatyolatyola mafupa anga onse;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

14. Ndinalankhula-lankhula ngati namzeze, pena cumba;Ndinalira maliro ngati nkhunda;Maso anga analephera pogadamira kumwamba.Yehova ndasautsidwa, mundiperekere cikoli.

15. Kodi ndidzanena ciani?Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wacita ici;Ine ndidzayenda cete zaka zanga zonse,Cifukwa ca zowawa za moyo wanga.

16. Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo.Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga;Cifukwa cace mundiciritse ine,Ndi kundikhalitsa ndi moyo.

17. Taonani, ndinali ndi zowawa zazikuru,Cifukwa ca mtendere wanga;Koma Inu mokonda moyo wanga,Munaupulumutsa m'dzanja la cibvundi,Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu macimo anga onse.

18. Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu;Imfa singakulemekezeni;Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.

19. Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero;Atate adzadziwitsa ana ace zoona zanu.

20. Yehova ndiye wondipulumutsa ine;Cifukwa cace tidzayimba nyimbo zanga, ndi zoyimba zazingweMasiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.

21. Ndipo Yesaya adati, Atenge mbulu wankhuyu, auike papfundo, Ndipo iye adzacira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 38