Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 38:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2. Ndipo Hezekiya analoza nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,

3. Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndacita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.

4. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,

5. Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.

6. Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.

7. Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;

8. taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.

9. Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atacira nthenda yace.

10. Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11. Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 38