Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 37:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali pamene mfumu Hezekiya anamva, anang'amba zobvala zace, nabvala ciguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova.

2. Ndipo anatumiza Eliakimu, wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi akuru a nsembe, atapfunda ciguduli, kwa Yesaya, mneneri, mwana wa Amozi.

3. Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la bvuto, ndi lakudzudzula, ndi citonzo; pakuti nthawi yace yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira.

4. Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asuri mbuyace inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; cifukwa cace, kweza pemphero lako cifukwa ca otsala osiyidwa.

5. Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya.

6. Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asuri andilalatira Ine.

7. Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao.

8. Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asuri irikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inacoka ku Lakisi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 37