Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 37:21-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Popeza wandipemphera za Sanakeribu mfumu ya Asuri,

22. awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi ciphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wace pambuyo pako.

23. Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? ndiye Woyera wa Israyeli.

24. Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magareta anga ine ndafika ku nsonga za mapiri, ku mbali za Lebano; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pace penipeni, ku nkhalango ya munda wace wobalitsa.

25. Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa nyanja zonse za Aigupto ndi kuphazi kwanga.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 37