Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 36:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asuri itere, Mupangane nane, turukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zace, ndi nkhuyu zace, namwe yense madzi a pa citsime cace;

17. kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu ku dziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la cakudya ndi minda yamphesa.

18. Cenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iri yonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asuri?

19. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu? kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga?

20. Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?

21. Koma iwo anakhala cete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.

22. Ndipo anafika Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 36