Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 35:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa.

2. Lidzaphuka mocuruka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukuru wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukuru wace wa Mulungu wathu.

3. Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.

4. Nenani kwa a mitima ya cinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera cilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.

5. Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa.

6. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba; pakuti m'cipululu madzi adzaturuka, ndi mitsinje m'dziko loti se.

7. Ndipo mcenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu.

8. Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzachedwa njira yopatulika; audio sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasocera m'menemo.

9. Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale cirombo colusa sicidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m'menemo,

10. ndiro oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuyimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo cisoni ndi kuusa moyo kudzacoka.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 35