Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 31:7-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ace asiliva, ndi mafano ace agolidi amene manja anu anu anawapanga akucimwitseni inu.

8. Pamenepo Asuri adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammariza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ace adzalamba.

9. Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 31