Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu.