Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 3:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? ati Ambuye Yehova wa makamu.

16. Komanso Yehova ati, Cifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;

17. cifukwa cace Ambuye adzacita nkanambo pa liwombo la ana akazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzabvundukula m'cuuno mwao.

18. Tsiku limenelo Ambuye adzacotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande;

19. mbera, ndi makoza, ndi nsaru za pankhope;

20. ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri;

21. mphete, ndi zipini;

22. malaya a paphwando, ndi zopfunda, ndi zimbwi, ndi timatumba;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 3